15 Mfumu inalamula kuti operekera makalatawo apite mwamsanga.+ Lamuloli linaperekedwa mʼnyumba ya mfumu ya ku Susani+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Kenako mfumu ndi Hamani, anakhala pansi nʼkumamwa vinyo, koma mumzinda wa Susani munali chipwirikiti.