9 Tsiku la 13 la mwezi wa 12, umene ndi mwezi wa Adara,+ linali tsiku limene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinayenera kuchitika.+ Limeneli linali tsiku limene adani a Ayuda ankayembekezera kugonjetsa Ayudawo. Koma pa tsikuli zinthu zinasintha, moti Ayuda ndi amene anagonjetsa adani awowo.+