11 Azichimwene ndi azichemwali ake onse komanso anzake onse akale+ anapita kwa iye ndipo anadya naye limodzi chakudya mʼnyumba mwake. Iwo anamulimbikitsa komanso kumupepesa chifukwa cha masoka onse amene Yehova analola kuti amugwere. Aliyense wa iwo anamupatsa ndalama ndi mphete yagolide.