-
Yesaya 9:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Komabe mdima wake sudzakhala ngati wa pa nthawi imene dzikolo linali mʼmavuto, ngati kale pamene anthu ankanyoza dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali.+ Koma pakadzapita nthawi, Mulungu adzachititsa kuti anthu alemekeze dzikolo, dera limene kuli njira yamʼmphepete mwa nyanja, mʼchigawo cha Yorodano, ku Galileya kumene kunkakhala anthu a mitundu ina.
-