18 Koma phindu lake ndi malipiro akewo zidzakhala zopatulika kwa Yehova. Zinthu zimenezi sizidzasungidwa kapena kuikidwa pambali, chifukwa malipiro akewo adzakhala a anthu okhala pamaso pa Yehova, kuti anthuwo azidya mpaka kukhuta ndiponso kuti azivala zovala zokongola.+