22 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Taona! Ineyo ndidzakwezera dzanja langa mitundu ya anthu,
Ndipo anthu a mitundu ina ndidzawakwezera chizindikiro.+
Iwo adzakubweretsera ana ako aamuna atawanyamula mʼmanja,
Ndipo ana ako aakazi adzawanyamula paphewa.+