6 Mneneri Yeremiya anayankha kuti: “Zikhale momwemo! Yehova achitedi zimenezo! Yehova akwaniritse mawu ako amene walosera. Achite zimenezo pobwezeretsa pamalo ano ziwiya zamʼnyumba ya Yehova ndi anthu onse amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo!