3 Ndiyeno akalonga onse a mfumu ya Babulo analowa mumzindawo nʼkukhala pansi pa Geti la Pakati.+ Mayina awo anali Nerigali-sarezera amene anali Samugari, Nebo-sarisekimu amene anali Rabisarisi, Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi ndi akalonga ena onse a mfumu ya Babulo.