16 “Pita kwa Ebedi-meleki+ wa ku Itiyopiya ndipo ukamuuze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Taona! Ndikukwaniritsa mawu anga akuti mzinda uwu ndidzaugwetsera tsoka osati zinthu zabwino ndipo pa tsikulo iweyo udzaona zimenezi zikuchitika.”’