-
Yeremiya 41:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Isimaeli anagwira anthu ena onse amene anali ku Mizipa,+ kuphatikizapo ana aakazi a mfumu ndi anthu ena onse amene anatsala ku Mizipa omwe Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anawapereka kwa Gedaliya+ mwana wa Ahikamu kuti aziwayangʼanira. Isimaeli mwana wa Netaniya anawagwira ndipo ananyamuka kuti awolokere nawo kudziko la Aamoni.+
-