8 Nʼchifukwa chiyani mukufuna kundikhumudwitsa ndi ntchito za manja anu popereka nsembe kwa milungu ina mʼdziko la Iguputo kumene mwapita kuti muzikakhala? Muwonongedwa ndipo aliyense azidzakutembererani ndi kukunyozani pakati pa anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi.+