23 Masoka onsewa akugwerani ngati mmene ziliri lero chifukwa chakuti munkapereka nsembe zimenezi komanso chifukwa chakuti munachimwira Yehova. Munachita zimenezi polephera kumvera mawu a Yehova, kutsatira malamulo ake, malangizo ndi zikumbutso zake.”+