-
Ezekieli 11:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 “Iwe mwana wa munthu, abale ako enieni, azichimwene ako amene ali ndi ufulu wowombola, limodzi ndi nyumba yonse ya Isiraeli, auzidwa ndi anthu amene akukhala ku Yerusalemu kuti, ‘Pitani kutali ndi Yehova. Dzikoli ndi lathu. Laperekedwa kwa ife kuti likhale lathu.’
-