19 Koma mudzanena kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwanayo alibe mlandu uliwonse pa zolakwa za bambo akewo?” Popeza kuti mwanayo anachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo, anasunga malamulo anga onse komanso kuwatsatira, ndithu iye adzapitiriza kukhala ndi moyo.+