41 Chifukwa cha kafungo kosangalatsa, ndidzasangalala nanu ndikadzakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina nʼkukusonkhanitsani pamodzi kuchokera mʼmayiko osiyanasiyana kumene munabalalikira.+ Komanso ndidzakusonyezani kuti ndine woyera ndipo anthu a mitundu ina adzaona zimenezi.+