24 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Mwachititsa kuti zolakwa zanu zikumbukiridwe. Mwachita zimenezi poonetsa poyera zolakwa zanuzo komanso pochititsa kuti machimo anu aoneke mʼzochita zanu zonse. Tsopano popeza mwakumbukiridwa, adzakutengani mokakamiza.’