12 Iye ankalakalaka kwambiri kugona ndi amuna amʼdziko la Asuri+ omwe anayandikana nawo. Amuna amenewa anali abwanamkubwa ndi achiwiri kwa olamulira amene ankavala zovala zokongola ndipo anali akatswiri okwera mahatchi. Onsewa anali anyamata osiririka.