26 Kumeneko nʼkumene kuli Meseki ndi Tubala+ limodzi ndi magulu a anthu awo onse amene ankawatsatira. Manda awo ali mozungulira mfumu yawo. Onsewa ndi anthu osadulidwa, anthu amene anabaidwa ndi lupanga chifukwa anachititsa kuti anthu amene akukhala mʼdziko la anthu amoyo azikhala mwamantha.