27 Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, anthu amene akukhala mʼmabwinja adzaphedwa ndi lupanga. Amene ali kutchire ndidzawapereka kwa zilombo zolusa kuti akhale chakudya chawo. Ndipo amene ali mʼmalo otetezeka komanso mʼmapanga adzafa ndi matenda.+