13 Nkhosa zanga ndidzazitulutsa pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzazisonkhanitsa pamodzi kuchokera mʼmayiko ena nʼkuzibweretsa mʼdziko lawo. Ndidzazidyetsa mʼmapiri a ku Isiraeli,+ mʼmphepete mwa mitsinje komanso pafupi ndi malo onse amʼdzikolo kumene kumakhala anthu.