3 Choncho losera ndipo unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Adani anu akusandutsani bwinja ndipo akuukirani kuchokera kumbali zonse. Achita zimenezi kuti anthu a mitundu ina amene anapulumuka akutengeni kuti mukhale awo ndipo anthu akunena za inu komanso kukunenerani miseche.+