9 Kenako anandiuza kuti: “Losera kwa mphepo. Iwe mwana wa munthu, losera ndipo uuze mphepoyo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe mphepo, bwera kuchokera kumbali zonse 4 nʼkuwomba anthu amene anaphedwawa kuti akhalenso ndi moyo.”’”