3 Nyumbayi inali pakati pa bwalo lamkati lomwe linali mikono 20 mulifupi+ ndi malo owaka miyala amʼbwalo lakunja. Panali nyumba ziwiri zoyangʼanizana, zomwe zinali ndi zipinda zodyera. Nyumbazo zinali zosanjikizana katatu ndipo zinali ndi makonde omwe anali moyangʼanizana.