8 Iwo anaipitsa dzina langa loyera chifukwa cha zinthu zonyansa zimene anachita pamene anaika khomo lawo pafupi ndi khomo langa, nʼkuika felemu la khomo lawo pafupi ndi felemu la khomo langa moti pakati pa iwowo ndi ine nʼkungokhala khoma lokha lotisiyanitsa.+ Choncho ndinawawononga nditakwiya.+