-
Ezekieli 46:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Mukamapereka mwana wa nkhosayo, muziperekanso nsembe yambewu mʼmawa uliwonse yokwanira gawo limodzi mwa magawo 6 a muyezo wa efa. Muziperekanso mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini kuti aziwazidwa mu ufa wosalala monga nsembe yambewu imene iziperekedwa kwa Yehova nthawi zonse. Limeneli ndi lamulo limene lidzakhalepo mpaka kalekale.
-