17 Koma akapereka mphatso kwa mmodzi wa antchito ake kuchokera pacholowa chake, mphatsoyo idzakhala ya wantchitoyo mpaka chaka cha ufulu,+ kenako idzabwezedwa kwa mtsogoleriyo. Koma cholowa chimene wapereka kwa ana ake chidzakhala chawo mpaka kalekale.