20 Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Awa ndi malo amene ansembe aziwiritsirapo nsembe yakupalamula ndi nsembe yamachimo komanso pamene aziphikirapo nsembe yambewu.+ Aziphikira pamenepa kuti asamatulutse chilichonse kupita nacho kubwalo lakunja nʼkuchititsa kuti anthu akhale oyera.”+