9 Kulikonse kumene madziwo apita, zamoyo zamʼmadzi za mtundu uliwonse zidzakhala ndi moyo. Nsomba zidzachuluka chifukwa madzi amenewa adzafika kunyanja. Madzi amʼnyanja adzakhala abwino ndipo kulikonse kumene mtsinjewo ukupita, chilichonse chidzakhala ndi moyo.