5 Kuwonjezera pamenepo, mfumu inalamula kuti tsiku lililonse aziwapatsa zakudya zabwino za mfumu ndi vinyo wofanana ndi amene mfumu inkamwa. Ankayenera kuwaphunzitsa kwa zaka zitatu ndipo pambuyo pa zaka zimenezi, ankayenera kuyamba kutumikira mfumu.