23 Ndiyeno iye anandiuza kuti: ‘Ponena za chilombo cha nambala 4 chimenechi, pali ufumu wa nambala 4 umene udzakhalepo padziko lapansi. Udzakhala wosiyana ndi maufumu ena onse ndipo udzadya dziko lonse lapansi komanso udzalipondaponda nʼkuliphwanyaphwanya.+