4 Ndinaona nkhosa yamphongoyo ikuukira adani ake kumadzulo, kumpoto ndi kumʼmwera ndipo palibe zilombo zakutchire zimene zinalimbana nayo komanso palibe amene akanakwanitsa kupulumutsa aliyense ku mphamvu zake.+ Nkhosayo inkachita zofuna zake ndipo inkadzitama kwambiri.