-
Danieli 11:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Pakadzatha zaka zingapo iwo adzapanga mgwirizano ndipo mwana wamkazi wa mfumu yakumʼmwera adzapita kwa mfumu yakumpoto kuti apange mgwirizano. Koma mwana wamkaziyo sadzakhalanso ndi mphamvu ndipo mphamvu za mfumuyo zidzathanso. Mwana wamkaziyo adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu ena pamodzi ndi amene anamubweretsa, amene anamubereka ndiponso amene ankamuchititsa kukhala wamphamvu masiku amenewo.
-