7 Kenako munthu wina wochokera ku mphukira ya mizu ya mwana wamkaziyo adzayamba kulamulira mʼmalo mwake ndipo adzafika kwa gulu lankhondo nʼkupita kukaukira mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri wa mfumu yakumpoto, moti munthuyo adzachita nayo nkhondo nʼkupambana.