15 Kenako mfumu yakumpoto idzabwera ndipo idzamanga malo okwera omenyerapo nkhondo nʼkulanda mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Zida zankhondo zakumʼmwera komanso asilikali ake osankhidwa mwapadera sadzatha kulimbana ndi mfumuyo. Iwo sadzakhala ndi mphamvu zoti alimbane nayo.