40 Mu nthawi yamapeto mfumu yakumʼmwera idzayamba kukankhana ndi mfumu yakumpoto ndipo mfumu yakumpotoyo idzabwera mwamphamvu kudzamenyana nayo. Idzabwera ndi magaleta, asilikali okwera pamahatchi ndi sitima zambiri zapamadzi ndipo idzalowa mʼmayiko nʼkudutsamo mofulumira ngati madzi osefukira.