-
Yoweli 2:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Limeneli ndi tsiku lamdima ndi lachisoni,+
Tsiku lamitambo ndi lamdima wandiweyani.+
Tsikuli lili ngati mmene kuwala kwa mʼbandakucha kumaonekera pamwamba pa mapiri.
Pali mtundu wa anthu ambiri ndiponso amphamvu.+
Kuyambira kalekale, palibenso mtundu wina womwe ungafanane nawo,
Ndipo sikudzakhalanso mtundu wina wofanana nawo,
Kumibadwomibadwo.
-