17 Ndiyetu Yehova wanena kuti: “Mkazi wako adzakhala hule mumzindawu. Ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa ndi lupanga. Anthu adzagawana dziko lako mochita kuyeza ndi chingwe, ndipo iweyo udzafera mʼdziko lodetsedwa. Isiraeli adzagwidwa ndithu mʼdziko lake nʼkutengedwa kupita ku ukapolo.”’”+