16 kodi zinthu zinali bwanji? Munthu ankati akapita pamulu wa zokolola umene ukanakwana miyezo 20, ankapeza kuti ndi wongokwana miyezo 10. Ndipo munthu ankati akapita moponderamo mphesa kuti akatunge miyezo 50 ya vinyo, ankapeza kuti muli wongokwana miyezo 20.+