13 Mumanenanso kuti, ‘Koma ndiye nʼzotopetsa bwanji!’ Ndipo mumanunkhiza nsembezo monyansidwa,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. “Inu mumabweretsa nyama zobedwa, zolumala ndi zodwala. Mumabweretsa zimenezi ngati mphatso. Kodi ine ndingalandire nsembe zoterezi?”+ watero Yehova.