36 Komanso anawapatsa fanizo lakuti: “Palibe amene amadula chigamba pamalaya akunja atsopano nʼkuchisokerera pamalaya akunja akale. Munthu akachita zimenezo, chigamba chatsopanocho chimachoka pansalu yakaleyo. Ndiponso chigamba cha nsalu yatsopanocho sichigwirizana ndi malaya akalewo.+