-
Luka 6:42Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
42 Ungauze bwanji mʼbale wako kuti, ‘Mʼbale taima ndikuchotse kachitsotso kamene kali mʼdiso lako,’ pamene iwe ukulephera kuona mtanda wa denga la nyumba umene uli mʼdiso lako? Wachinyengo iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba umene uli mʼdiso lakowo. Ukatero udzatha kuona bwino, moti udzakwanitsa kuchotsa kachitsotso kamene kali mʼdiso la mʼbale wako.
-