21 Koma anthu onse amene anamumva akulankhula, anadabwa kwambiri ndipo ankanena kuti: “Kodi munthu uyu si uja ankazunza anthu a ku Yerusalemu oitana pa dzina limeneli?+ Kodi chimene anabwerera kuno si kudzagwira anthu nʼkupita nawo kwa ansembe aakulu?”+