22 Iwo anati: “Tachokera kwa Koneliyo,+ mtsogoleri wa asilikali. Iye ndi munthu wolungama komanso woopa Mulungu ndipo mtundu wonse wa Ayuda umamuyamikira. Mngelo woyera anamupatsa malangizo ochokera kwa Mulungu kuti atume anthu kudzakutengani kuti mupite kunyumba kwake, akamve zimene inu mukanene.”