19 Herode anafunafuna Petulo paliponse ndipo atalephera kumupeza, anapanikiza alonda aja ndi mafunso komanso analamula kuti awatenge nʼkukawapatsa chilango.+ Kenako Herode anachoka ku Yudeya nʼkupita ku Kaisareya, komwe anakhalako kwakanthawi ndithu.