20 Herode anakwiyira kwambiri anthu a ku Turo ndi ku Sidoni. Choncho anthuwo anabwera kwa iye mogwirizana ndipo atamunyengerera Balasito, amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu, anapempha mtendere. Iwo anachita zimenezi chifukwa dziko lawo linkadalira chakudya chochokera mʼdziko la mfumuyo.