14 Pagululo panali mayi wina dzina lake Lidiya ndipo anali wolambira Mulungu. Iye ankachokera mumzinda wa Tiyatira+ ndipo ankagulitsa nsalu ndi zovala zapepo. Pamene ankamvetsera, Yehova anatsegula kwambiri mtima wake kuti amvetse zimene Paulo ankalankhula.