5 Koma Ayuda anachita nsanje+ ndipo anasonkhanitsa anthu ena oipa amene ankangokhala pamsika. Iwowa anapanga gulu lachiwawa nʼkuyambitsa chipolowe mumzindamo. Kenako anapita kunyumba ya Yasoni, kukafuna Paulo ndi Sila kuti awatulutse nʼkuwapereka ku gulu limene linkachita chipolowelo.