14 Koma chomwe ndikuvomereza kwa inu ndi chakuti: Njira yolambirira imene iwo akuitchula kuti ‘gulu lampatuko,’ ndi imene ine ndikuitsatira potumikira Mulungu wa makolo anga.+ Chifukwa ndimakhulupirira zonse zimene zili mʼChilamulo ndi zimene aneneri analemba.+