11 Ngati ndilidi wolakwa, ndipo ndikuyenera kuphedwa chifukwa cha zimene ndachita,+ sindikukana kufa. Koma ngati zimene akundinenezazi ndi zosamveka, palibe munthu amene angandipereke kwa iwo kuti awasangalatse. Ndikuchita apilo kuti ndikaonekere kwa Kaisara.”+