17 Patatha masiku atatu, Paulo anaitanitsa akuluakulu a Ayuda. Atasonkhana, anawauza kuti: “Amuna inu, abale anga, ngakhale kuti sindinachite chilichonse chotsutsana ndi anthu kapena mwambo wa makolo athu,+ anandigwira ku Yerusalemu nʼkundipereka mʼmanja mwa Aroma ngati mkaidi.+